PHUNGU WA ZOMBA MALOSA WAPEMPHA BOMA KUTI LITHANDIZE MKAZI WAMALEMU COLONEL OWEN SAMBALOPA PAMODZI NDI ANA.
Mkazi wa malemu Col. Owen Salambalopa

PHUNGU WA ZOMBA MALOSA WAPEMPHA BOMA KUTI LITHANDIZE MKAZI WAMALEMU COLONEL OWEN SAMBALOPA PAMODZI NDI ANA.

Phungu wakunyumba yamalamulo mdera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta wapempha Boma kuti lithandize nkazi wamalemu Colonel Owen Sambalopa pamodzi ndi ana chifukwa pakali pano alibe mtengo ogwira popedza munthu yemwe amamudalira pabanja lawo adamwalira pangozi yandege akugwira ntchito.

Sambalopa adamwalira pangozi ya ndege ku Chikangawa boma la Mzimba pamodzi ndi wachiwiri kwa pulezidenti malemu Dr. Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi awiri.

Kwelepeta wapemphanso Boma kuti lilembe ntchito ana awiri kapena mmodzi amalemu Colonel Sambalopa kuti azitha kuthandiza mai awo komanso achibale awo pankhani yamaphunziro.

Phunguyu wati ngati phungu wakunyumba yamalamulo mdera la Zomba Malosa komwe malemu Colonel Sambalopa amachokera ali ndichisoni chachikulu chifukwa cha ifa imeneyi yomwe pakali pano ilibe mayankho.

Kwelepeta adatinso ngakhale malemu Colonel Sambalopa ankagwira ntchito ku Malawi Defense Force koma adalinso kuthandiza nawo nkhani zachitukuko mdera la Zomba Malosa ndipo mwachisanzo adati nthawi yomwe mdera lake lidakhudzidwa ndi Cyclone Freddy adatenga nawo gawo lalikulu lothandiza anthu okhudzidwa.

“Langa ndipempho lopita ku boma kuti lichite chothekera kuti lithandize nkazi wamalemu Colonel Owen Sambalopa ndipo ngati nkotheka lilembenso ntchito ana amalemuwa kuti azitha kuthandiza mai awo.” watero Kwelepeta.

Malemu Colonel Owen Sambalopa yemwe adali katswiri oyendetsa ndege adamwalira pangozi yandege pamodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Dr Saulosi Klaus Chilima yomwe idagwa munkhalango ya Chikangawa.

Kutsatira ngoziyi Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera adalamula kuti dziko lino likhuze malirowa kwa masiku masabata atatu

Kuonjezera apo Pulezident Chakwera adaimitsanso ulendo omwe amayembekezera kupita dziko lw South Africa komwe kudali mwambo wolumbiritsa Pulezidenti Cyril Ramaphosa kutsatira kusankhidwa kwake pa chisankho chomwe chidachitika mdzikolo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *