Denis Namachekecha
Denis Namachekecha

BUDGET NDI YOFUNIKA WOSAMAITENGERA NDALE- NAMACHEKECHA

Phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la ku Mpoto kwa Phalombe a Denis Namachekecha ati ndi wokondwa kuti ndondomeko ya za chuma ya 2025-2026 yadutsa nyumba ya malamulo.

Anamachekecha amathilila ndemanga maka poona kuti pali zithu zambiri dziko muno zomwe zinaima podikila kuti  ndondomeko idutse Kaye.

Iwo anati akhala akuima nyumba ya malamulo kupepha ku unduna wa za maphunziro Kuti ulembe ntchito aphunzitsi magulu anayi omwe akhala akupanga maphunziro koma wosalembedwa ntchito.

“Ndakhala ndipepha nyumba ya malamulo mwina kopitilira kawiri kuti uduna wa za chuma uike ndalama zolembera aphunzitsi omwe achita maphunziro awo koma sakulembedwa ntchito, zomwe anduna a zachuma anati zili mu ndondomeko ya za chuma kale, ndipo ndine wokondwa kuti ndaona Kuti ndalama pafupi fupi 10 billion zaikidwamo.” Anatero Anamachekecha.

Iwo anapitiliza kunena Kuti ndondomeko ya za chuma sichithu chopangira ndale chifukwa chimayang’ana zithu zambiri maka kwa anthu omwe timawaimilira kuno ku nyumba ya malamulo.

“Tisamalowetse ndale ngati m’mene zinkakhalira mbuyomu zomati section 65 first, budget second, uku ndi kuononga dziko lomwe anthu ake tikuwaimilira ndife”.

Ndondomeko ya Boma imayang’ana zithu monga nkhani ya zaumoyo, za ulimi, za maphunziro, za Miseu, ma salary aanthu wogwira ntchito Boma mwa zina.

Ndondomeko ya 2025-2026 muli ndalama zokwana 8.5 Trillion Malawi kwacha.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *