FAM YATOLERA NDALAMA ZOKWANA K126 MILIYONI PA MASEWERO A CHARITY SHIELD 

FAM YATOLERA NDALAMA ZOKWANA K126 MILIYONI PA MASEWERO A CHARITY SHIELD 

Zatsimikizika tsopano kuti zinthu zayamba kuyenda bwino mmzipata zotolera ndalama mma bwalo azamasewero kutsatira ndalama zomwe zapezeka pa masewero a charity shield amene anachitika pakati pa team ya Silver strikers ndi Mighty Wonders loweruka sabata yatha pa bwalo lazamasewero la Bingu.

Tulipo Mwenelupembe oyang’anira ntchito za malonda ku bungwe la Football Association of Malawi wati, ndalama zokwana K126,000,000.00 ndizomwe zapezeka pamasewerowa, zomwe akuti  zasintha kufanizira ndi mmbuyomu pomwe kumachuluka zochitika zambiri zachinyengo zimene zimasokoneza ndalama.

Iye wati akhala akukhwimitsa chitetezo mmalo onse otolera ndalamazi mmageti ammabwalo onse mdziko muno pamene maswero akuyamba loweruka likubwerali mzigawo zonse zadziko lino.

Timu ya Silver Strikers yavomereza kuti ikaswerera masewera awo ndi timu ya Bullets pa bwalo la zamasewero la Bingu pamene akukatsekulira ligi ya TNM kutsatira zokambirana zomwe zachitika ndi akuluakulu oyendetsa mpira wamiyendo.

Silver yati inali yodabwa kuti nchifukwa chiyani masewera awo apakhomo aikidwa bwalo la Bingu lomwe silawo pamene bwalo lawo lilibwinobwino ndipo lidavomerezedwa kuchititsa masewero alionse. 

Ronald Chiwaula wachiwiri Kwa mtsogoleri wa bungwe la SULOM  komanso Patrick Chimaimba woyendetsa timu ya Silver Strikers atsimikizira The Truth Malawi kuti izi zadza kutsatira zokambirana zomwe zinachitikazi pakati pawo.

Timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya atsikana inyamuka lero mdziko muno  kupita mdziko la South Africa komwe ikaswere masewero opimana mphamvu ndi timu ya Banyanabanyana pa 5 komanso pa 8 April 2025.

Lovemore Fazili mphunzitsi wa atsikanawa, wati masewerowa opimana mphamvuwa ndiwofunika kwambiri   pamene atsikanawa akuyembekera kusewera ndi timu ya Angola mumpikisano wa  Women Africa Cup of Nations mu mwezi wa October Chaka chino.

Fazili wati, akatswiri osewera kunja Kwa dziko lino monga Chimwemwe Madise, Vanessa Chikupira ndi Benedetta Mkandawire ndiomwe akhale nawo pamasewerowa.

Iwo ati osewera odalillika kwambiri monga Temwa Chawinga, mkuluwake Tabitha komanso Kabviele sapezeka nawo mmasewerawa omwe poyamba amkayembezeka kuseweredwa masabata awiri apitawa.

Masewera osiyanasiyana akhala akuchitika mmabwalo ambiri kutsatira kuyamba Kwa ligi ya TNM pa 5 April 2025.

Mmaswero akunja, Timu ya Man chester united yagonya ndi chigoli chimodzi Kwa duu mu English Primer League pamene anyamata a Arsenal apambana 2-1.

Timu ya Liverpool ili pa nambala yoyamba pomwe ili ndi ma points 70 itasewera masewero 29 pamene Arsenal yasewera masewero 30 ndipo ali ndi ma points 61 ndipo iwowa ali pa nambala yachiwiri.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *