UDF IPANGA MGWIRIZANO NDI A MALAWI WATERO ATUPELE MULUZI

UDF IPANGA MGWIRIZANO NDI A MALAWI WATERO ATUPELE MULUZI

Mtsogoleri wachipani cha UDF Atupele Muluzi loweruka watsimikizira anthu pa bwalo la Masintha mu mzinda wa Lilongwe kuti iye ndi chipani chake apanga mgwirizano ndi a Malawi kuti azapambane pa chisankho cha mu Sepitembala chaka chino.

Muluzi wanena izi kutsatira kupereka makalata ake ku bungwe loyendetsa chisankho la MEC ngati njira yotsimikizira anthu kuti wakonzeka kupukumutsa anthu ku mavuto.

Iye walonjeza kuchita kampeni wamphamve kuposa wina aliyense amene akufuna kupikisana nawo pa udindo wa upulezidenti mziko muno.

Mawu oti achita kampeni kuposa wina aliyense, akufanana ndi omwe adayankhula mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera pa tsiku lomwe amatsegulira kampeni ya chipani cha MCP ku bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.

Pa mnsonkhanowu, Muluzi wakhazikitsanso manifesto a chipanichi omwe wanena kuti akhala akuwatambasula akamataegulira kampeni masiku akubwerawa.

“Manifesto achipani cha UDF muli zinthu zitatu zomwe taziika kuti zizawachotse anthu ku mavuto omwe akukumana nawo monga Kukhala ndi pulani yokhazikika, kuchita zinthu pogwiritsa ntchito luso lanakono komanso kubwezeretsa chuma mchimake kuti chikhale chokhazikika”,adatero Muluzi.

Muluzi wati pali maiko angapo omwe ndi olemera kwambiri omwe posachedwapa abwera poyera kuvomereza mfundo zomwe UDF yakonza. Iye anatchula maiko monga United Arab Emirates, Saud Arabia mwa ena kuti wakumana kale ndi atsogoleri ake.

Iye walonjeza kusintha Malawi ndikuchilimika powamenyera nkhondo yothana ndi umphawi. Mtsogoleriyu wachenjezanso anthu kuti asavotere atsogoleri omwe ali kale ndi mbiri za katangale. Adalimbikitsanso achinyamata kuti achilimike popereka support kwa atsogoleri achinyamata monga Atupele Muluzi.

“UDF ndi chipani chokhacho chili ndi mbiri yochotsera pampando MCP chifukwa cha utsogoleri wake ochangamuka”,adatero Muluzi.

Pokapereka makalata ku bungwe loyendetsa chisankho la MEC mu mzinda wa Lilongwe, Muluzi adalengeza kuti a Dr. Lex Kalolo ndi omwe akhale wachiwiri wawo pa chisankho cha pa 16 September.

Bungwe la MEC lidayamba kulandira makalata kwa omwe akufuna kudzapikisana pa maudindo a khansala, phungu komanso pulezidenti pa 24 mwezi uno ndipo ntchitoyi idzatha pa 30 mwezi omwe uno.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *