OCHITA MALONDA KU MZUZU APEREKA KALATA YAMADANDAULO KU BUNGWE LA MRA

OCHITA MALONDA KU MZUZU APEREKA KALATA YAMADANDAULO KU BUNGWE LA MRA

Ochita malonda osiyanasiyana kuchigawo chakumpoto apereka kalata yawo yamadandaulo posutsana ndi njira yatsopano yotolorera msonkho ya Electronic Invoicing System(EIS) yomwe ati ndiyowaphinja.

Popereka kalata yamadandaulo ku bungwe lotolera misonkho la MRA, wapampando wa bungwe laochita malonda la Northern Business Community a Chembe Kasambara ati ndiwodandaula kamba kanjira yotolera msonkhoyi yomwe ati iwafinya pamalonda awo.

“Tikupempha kuti MRA iwunikirenso njirayi ndipo isagwiritsidwenso ntchito kuti tisafinyike pamisonkho.” Atero a Kasambala.

Polandira kalata yamadandauloyi m’modzi mwa akuluakulu ku ofesi ya MRA ku Mzuzu a Robert Nyirongo ati ayilandira kalatayi ndipo akayipereka kulikulu lawo.

Pakadali pano ochita malondawa omwe ndiochokera ku Mzuzu, Rumphi komanso ku Nkhatabay apereka masiku khumi kuti ayankhidwe pamadandaulo omwe apereka.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *