Wa pa mpando wa komiti ya Public Account committee (PAC) a Steve Baba Malondera wati ndi wokhumudwa ndi kagwilidwe ntchito ka Bungwe la MEDEF lomwe mbuyo limatchedwa kuti NEEF.
Iwo amayankhula izi pomwe bungweli linadzaonekera kunyumba ya malamulo pomwe limakuna ndi committee yomwe imalondoloza mu nyumba ya malamulo.
Mkulu wa MEDEF a Kaisi Msadala anati bungwe lawo lili ndi katundu wambiri yemwe akufuna kumugulitsa mu njira ya ndagwira popewa kuti angaonongeke komaso kuti wina abwezere ngongole zomwe alinazo zomwe iwo anakatenga ku makampani kwina.
Poyankhapo wa pa mpando wa committee yi a Steve Baba Malondera ati bungweli limagwira ntchito mwachibwana mosatsata malamulo chifukwa iwo ntchito yawo inali yobwereketsa ndalana wosati kumagula zipangizo za ulimi nkumabwereketsa anthu.
Iwo anapitiliza kunena kuti pa 100 Billion yonwe anapatsidwa ndi kuchoka kubungwe la zachuma akwanitsa kupeza 16, billion yonkha bas.Zomweso sanafotokoze kuti zitoleredwa bwanji, uku ndikuseweretsa chuma cha Boma.
” Pasanathe sabata imodzi tikuitanitsa a Treasurery kuti adzafokoze bwino bwino za mmene abayendetsera ndalama” anatero a Malondera.
Iwo ati zomwe likufuna kuchita bungwe la MEDEF kufuna kugulitsa zithu, akuyenera kusiira mmanja mwa PPDA kapena Small holder, kuti ayendetse ndondomeko.

