Nsonkhano wotsiliza wachipani cha People’s Party (PP) wachitika ku Namwela mdera la Senior Chief Malemia ku Zomba Malosa ndipo mtsogoleri wachipanichi Joyce Banda ndiyemwe akuyembekezeka kuyankhula kwa khwimbi la anthu omwe afika pamalowa.
Pakali pano yemwe akuna kuzayimira ngati Phungu wakunyumba yamalamulo mdera la Zomba Malosa Edith Kachale Banda anafika pamalowa pamodzi ndi mtsogoleri wachipani cha PP chigawo chaku mawa Lawrence Bisika.
Anthu ochuluka anafika pamalowa koma Joyce Banda sadafikebe pamalowa chifukwa akuchita misonkhano yoyima ima Boma la Machinga. Mau ake Edith Kachale Banda wapempha anthu kuti azapite mwa unyinji pa 16 September ndipo akamuvotere kuti azatukule mdera la Zomba Malosa.
Poyankhulapo mtsogoleri wachipanichi chigawo chaku mawa Lawrence Bisika wati dziko lino zinthu zofunika pamoyo wamunthu zakwera mtengo chifukwa cha utsogoleri osakonda anthu ake.


