Phungu wanyumba ya Malamulo wa Balaka Bwaira Dr Fletcher Luke Padoko m’boma la Balaka ati akukhulupilira kuti Boma la DPP kudzera mu utsogoleri wa Professor Urthur Peter Mutharika lithandiza kutukula dziko lino muzochitika zosiyanasiyana.
Izi amayankhula nyumba ya malamulo pamene amapepha nduna yoona za migodi ndi mphamvu za Magetsi a Jean Mathanga kuti alumikize magetsi mu School zisanu ndi ziwiri za mu delari.
A Dr Padoko ati school monga Mzimundilinde, Kaphilikwete, Makuta, Kasupe, Binoni, Magomero ndi Chikowa
“Mfundo za Mutharika ndi zofuna kuti town tsopano ipite kumudzi kuti anthu adzipeza mwayi wofanana ndi anthu Amatauni” anatero Dr Padoko.
Poyankhapo a Jean Mathanga nduna ya migodi ndi mphamvu za magetsi ati masukulu ena ali kale mundondomeko ya Malepu 9 ndi 10 zomwe ntchitoyi iyambe posachedwapa.
Dr Padoko ati akathana ndi Nkhani za magetsi akuyembekezera kuyamba ntchito yokoza nseu wa Balaka – Ulongwe, ndi Balaka – Kachenga.


