Ntchito zamalonda zidayamba zayima kaye mu mzinda wa Zomba Lachisanu mamawa chifukwa anthu ochita malonda mu mzindawu adatengana kukapereka kalata yamadandaulo ku Bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA).
Ochita malondawa adakapereka kalata yamadandauloyi ati posakondwa ndi njira yotchedwa Electronic Invoicing System yomwe Bungwe la MRA likufuna kukhadzikitsa kuyambira pa 1 February chaka chino.
Anthu ochita malondawa adayenda ulendo wandawala kuchokera pamalo omwetsera mafuta agalimoto a Puma mpaka kukafika kuma office a MRA omwe ndi mtunda osachepera ma meter 150.
Poyankhula atapereka chikalata chamadandaulocho wapampando wa ochita malonda mu mzinda wa Zomba Masauko Mandula wati ngati sayankhidwa madandaulo awo kufika Lachitatu sabata ikubwerayi ndiye kuti sazatsekula malo awo onse ochitira malonda.
“Zomwe likuchita bungwe la MRA likufuna kupha ntchito zamalonda muno Malawi, choncho ngati asatiyankhe madandaulo athu kuyambira sabata yamawa Lachitatu tizayamba tayima kaye kuchita malonda.” Iwo adatero.
Ndipo poyankhula atalandira chikalata chamadandaulocho Mkulu woona ntchito yotelera misonkho ku Office ya MRA mu Boma la Zomba Jane Maere adati akatatula chikalata chamadandaulocho kulikulu la Bungwe la MRA.
Pakali pano ntchito zamalonda zayambiranso mu mzinda wa Zomba


