ANTHU ATATU APEZEKA NDI KOLERA KU ZOMBA

ANTHU ATATU APEZEKA NDI KOLERA KU ZOMBA

Anthu atatu apezeka ndi matenda a cholera pachipatala cha Ngwelero Boma la Zomba.

Wofalitsa nkhani ku office yaza umoyo Boma la Zomba Arnold Mndalira ndiyemwe wayankhula izi ndi ntolankhani wathu.

Ndalira wati mwa anthu atatuwa awiri ndi amidzi yozungulira ndipo modzi ndiwochokera Boma la Mulanje koma amagwiritsa ntchito chipatala cha Ngwelero popeza chipatalachi chili malire amaboma awiriwa.

Iye wati matendawa abuka chifukwa anthuwa adadya zokudya zophika phika zomwe zidatsala kunsika.

Office yaza umoyo ikulangiza anthu kuti asamadye zokudya zosavinikira zomwe zinabwelera kumalonda ku nsika.

Mndalira wapempha anthu amdelari kuti akhale ndi zimbuzi za ukhondo komanso azizivinikira.

“Ife achipatala tidathamangirako ndipo tapereka maphunziro momwe angapewere nthendayi kwa anthu ozungulira.” Iye adatero.

Office yaza umoyo Boma la Zomba yapempha mamfumu komanso atsogoleri aminsika kuti aziwonetsetsa kuti zokudya zomwe zikumagulitsidwa zozikhala zovinikira kuwopetsa ntchentche.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *