Thupi la malemu Inspector Patricia Sipiliano yemwe adali wofalitsa nkhani ku Zomba Police Station aliyika mmanda Lachinayi ku Matawale mu mzinda wa Zomba.
Pamene nthawi imakwana 14.28 thupi la malemu Sipiliano lidali likulowa mmanda
Poyankhula pamwambo woyika mmanda thupi la malemu Sipiliano mmodzi mwa akulu akulu kunthambi ya Police Lena Maere adati malemu Sipiliano adali ozipereka pogwira ntchito yake komanso olimbikira.
Iye adati malamulo Sipiliano adayamba kugwira ntchito ngati wa Police pa 9 April chaka cha 2010 ndipo pamwene amamwalira adali adakwezedwa pa udindo wa Inspector.
Maere adati Police izamukumbukira Sipiliano chifukwa chokulimbikira kwake ntchito komanso ngati wofalitsa nkhani za a police adali kulumikizana bwino ndi atolankhani.
*Sipiliano adali ngati chikwangwani cha a Police kuno ku Zomba chifukwa ndiyemwe amafalitsa nkhani zone zochitika kuno.” Adatero Maere.
Malemu Patricia Sipiliano adabadwa pa 24 May 1986 ndipo wasiya mamuna.
Kumwambo osazikana ndi malemu Sipiliano kudali akulu akulu a nthambi ya Police monga Officer In Charge wa Zomba Police Station Deputy Commissioner Aubrey Kawale, Officer In Charge wa Police ya Machinga Assistant Commissioner Ireen Kaphamtengo komanso kudafika akulu akulu asilikari a Malawi Defense Force (MDF) mosogozedwa ndi Brigadier Simwaka.


