Mtsogoleri wotsutsa Boma nyumba ya Malamulo wa Chipani cha MCP a Simplex Chithyola Banda, ati SONA siyanakhe mafuso a Malawi maka pa nkhani ya zaulimi ndi ntchito kwa achinyamata mdziko muno.
Achithyola amayankhula izi nyumba ya Malamulo pomwe amayankha ndondomeko ya mmene dziko litayendere lachisanu lapitali potsegulira zokambira za aphungu lachisanu lapitali.
Achithyola ati mwa zina a Mutharika sananene pa momwe achinyamata angalembedwere ntchito mdziko muno popeza kuti akulimbikitsa maphunziro aulele kuti aliyense aphunzire.
Iwo anawonjezera kuti alimi ambiri akupitilira kusapeza phindu chifukwa akugula zipangizo za ulimi pa mitengo yokwera ndi kumagulitsa pamitengo yotsika zomwe zikulowetsa pansi ntchito za ulimi.
“Si cha nzeru kuti Boma lidzikagula chimanga dziko la Zambia pamene a Malawi ali ndi Chimanga chochukuka chifukwa chofuna kukhaulitsa mitundu ina dziko muno, kumeneko ndi kupha dziko” anatero a Chithyola.
Ndipo yemwe anayankhulira chipani cha UTM a Felix Njawala ati ndi zomvetsa chisoni kuti Malawi ngati dziko tikudalirabe ulimi wa mvula mu dzaka zino, pamene tili ndi mitsinje ya madzi ambiri pafupifupi mbari zonse za dziko muno.
Anjawala alangiza Boma la a Mutharika kuti liganizile za ulimi wa makono wa thilira kuti lithetse njala yomwe ikuphinja anthu ochuluka dziko muno.
“President wangoyankhula zomwe akuganizira koma wokwanilitsa ndifeyo ngati dziko moteto tikuyenera kugwirana manja” anatsindika moteto a Njawala.
Aphunguwa akhala akukambirana nyumbayi kufika pa 10 April.
Zateremu Nduna yoona za chuma a Josephy Mwanamvekha akuyembezereka kudzapereka ndondomeko ya za Chuma kunyumba ya Malamulo Friday pa 27 February.


