George Chaponda during press briefing

CHIPANI CHA DPP CHAYITANA ZIPANI ZA AFORD, UTM NDI UDF KU MSONKHANO WAKE WAUKULU

Chipani chachikulu chotsutsa mziko la Malawi cha Democratic Progressive Party (DPP) chanena kuti chaitana akuluakulu azipani zina zotsutsa ku msonkhano wake omwe ukuyembekezereka kuchitika kumathero a sabata ino.

Msonkhanowu ukachitikita ku COMESA mu mzinda wa Blantyre kuyambira pa 17 mpaka pa 18 mwezi uno.

Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa msonkhanuwu a George Chaponda atsimikiza izi pa msonkhano wa atolankhani zulo pomena kuti akufuna zipanizi zizaonelele nawo.

Mneneri wachipani cha UTM a Felix Njawala atsimikiza kuti alandira Kalata ya kuyitanidwaku.

Malinga ndi a Chaponda, nthumwi zosachepera 2, 600 zikuyembekezera kukumana ndi kusankha atsogoleri atsopano oyendetsa chipanichi kwa zaka zisanu zikubwerazi.

Iwo ati palibe membala yemwe waonetsa chidwi chozapikisana nawo pa mpando wa pulezidenti kupatula a Peter Mutharika 

“Udindo wa mtsogoleri wachipanichi ukuyenera kudzapita kwa  yemwe akutsogolera chipanichi pakadali pano Prof. Peter Mutharika popanda opikisana naye”, adatero Chaponda.

Iye adaonjezera kuti mwayi wapatsidwa kwa mamembala achopanich kupikisana pa udindo uliwonse omwe akuufuna ngati ali ndi zomuyenereza.

Zisankho zosankha atsogoleri ku msonkhanuwu zidzatsogoleleredwa ndi bungwe loyendetsa zisankho mziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC).

Uwu ukhala msonkhano waukulu wachiwiri kuchitika mziko muno pokonzekera zosankha za patatu za chaka cha mawa kutsatira msonkhano wa chipani Cha MCP.

Izi zikutanthauza kuti a Peter Mutharika akuyembekezera kuzapikiaana kwambiri ndi a Lazarus Chakwera a MCP yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino.

Zina mwa zipani zomwe zikuyembekezera kuchititsa msonkhano wosankha atsogoleri ndi monga UTM, PP, UDF komanso AFORD.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *