MCP SIYIKUTULUKANSO M’BOMA- WATERO CHAKWERA

MCP SIYIKUTULUKANSO M’BOMA- WATERO CHAKWERA

Mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa Chipani cholamula cha Malawi Congress Party (MCP) a Dr. Lazarus Chakwera wanenetaa kuti chipani chake sichikutuluka m’boma pompano.

Poyankhula loweruka pamene amatsekera mnsonkhano waukulu wa chipanichi ku Lilongwe, a Chakwera adati iye akhala akulamulira dziko lino mpaka 2030.

Iye wati akuona mmene anthu mzigawo zonse za dziko lino akumulimbikitsira pa ntchito ya chitukuko kidzera mu masankho omwe achitika zaka zinayi zapitazi.

“Chipani chathu chokondedwa cha MCP chakhala chikupambana zisankho zachinwereza mziko muno kuposa chipani china chilichonse ndipo zichitikanso chimodzimodzi mu zisankho za chaka cha mawa”, watero Chakwera.

Iye adaonjezera kuti idzapambana pa mpando wa pulezidenti, a phungu ndi ma khansala.

Mtsogoleriyu adalimbikitsa umodzi ndi kugwira ntchito molimbika pakati pa mamembala a chipanichi kuti adzawine chisankho cha 2025.

Chakwera adlengezanso kuti nkhomo ku chipanichi ndi lotsegula kwa omwe akufuna kuthandizana naye kutukula dziko lino.

Nthawi ya komveshioniyi, nthumwi kuchipanichi zinasankha a Chakwera amene analibe opikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa chipanichi.

Maudindo ena omwe anasankhidwa ndi monga awa:

1. Wachiwiri woyamba Mayi Catherine Gotani Hara

2. Mlembi wamkulu ndi Richard Chimwendo Banda

3. Msungichuma wa mkulu John Paul

4. Ofalitsa nkhani muchipanichi ndi Mayi Jessie Kabwira

5. Mkulu wa amayi ndi Mayi Jean Sendeza

6. Mkulu wachinyamata ndi Baba Steve Malondera komanso

7. mkulu woona za malamulo ndi Jivason Kazipatike.

Chipanichi chikuyenera kusankha maudindo ena mozogozedwa ndi atsogoleri a mzigawo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *