MIA WALAMULA KUFULUMOZITSA NTCHITO YOLUMIKIZA MADZI MWA ULELE

MIA WALAMULA KUFULUMOZITSA NTCHITO YOLUMIKIZA MADZI MWA ULELE

Nduna yoona za Madzi ndi Ukhondo Abida Mia walamula mabungwe onse a za madzi mziko muno kuti afulumizitse ntchito yolumikiza madzi kwa anthu mwa ulele.

A Mia adanena izi pa mwambo wokhazikitsa sabata ya ukhondo kwa Chinsapo mu mzinda wa Lilongwe.

Mwambowu idachitika tsiku limodzi ndi mwambo wokumbukira kusamba mmanja wa pa dziko lonse.

“Ndi thandizo la zachuma lochokwera ku banki yaikulu pa dziko lonse la pansi (World bank) mabungwe owoona za madzi mziko muno mukuyenera kuonetsetsa kuti anthu onse omwe adalembera kuti alumikizilidwe madzi mwa ulele athandizidwe,” adatero Mia.

Mkulu wa bodi yogawa madzi ya Blantyre Joe Ching’ani wati bungwe lawo ndi lozipereka kulumikiza ma kasitomala ake kuzera mu ndondomeko ya uleleyi.

Pa tsikuli, Mia adatsogolera anthu posesa komanso adapereka zipangizo zoikamo madzi ndi sopo ku sukulu ya pulayimale ya Chinsapo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *