AKHRISTU AMIPINGO YA KATOLIKA NDI ANGLICAN ACHITA NJIRA YAMTANDA MOGWIRIZANA.

AKHRISTU AMIPINGO YA KATOLIKA NDI ANGLICAN ACHITA NJIRA YAMTANDA MOGWIRIZANA.

Akhristu mazana mazana ampingo wakotolika a St Charles Lwanga Parish mogwirizana ndi akhristu a St George’s Anglican Parish mu mzinda wa Zomba adayenda njira yamtanda kukumbukira ifa ya Ambuye Yesu.

Njira yamtandayi idayambira ku St Charles Lwanga Parish mpaka kukafika ku St George’s Anglican Parish motsogezedwa ndi Bambo Mfumu Antonio Chidumu ampingo wakotolika ndi Bambo Christopher Mizaya ampingo wa Anglican.

Ansembe, asisitere, oyimira akhristu eni ake, wachiwiri kwa mfumu ya mzinda wa Zomba Khansala Anthony Gonani komanso oyimilira Bwana Nkubwa wa Boma la Zomba adayala nkhata zawo pamalo pomwe adayikapo mtanda.

Poyankhula pamwambowo Bambo Christopher Mizaya adayamikira mgwirizano wabwino omwe ulipo pakati pa mpingp wa Anglican ndi mpingo Wakatolika.

Iwo adapempha akhristu amipingo iwiriyi kuti azipemphelerana komanso apemphelere dziko la Malawi pamene likupita kuchisankho chosankha atsogeleri adziko.

Mau ake Bambo Chidumu adapempha akhristu kuti ngakhale angakumane ndi mavuto azilimbikira kupemphera ndipo athokoza akhristu chifukwa choyenda njira yamtanda.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *