MWANAMVEKA AKUFUNA A CHITHYOLA APEREKE UMBONI PA NKHANI YA IMF

MWANAMVEKA AKUFUNA A CHITHYOLA APEREKE UMBONI PA NKHANI YA IMF

Nduna ya Zachuma a Josephy Mwanamvekha yatsutsa phekesera zomwe tsogoleri wotsutsa Boma nyumba ya malamulo a Simplex Chithyola Banda anayankhula nyumbayi kuti Boma lasainilana gwilizano ndi Bank ya IMF kuti isalembenso achinyamata ntchito, komanso kukweza maudindo anthu ogwira ntchito m’boma, ndi kugwetsa ndalama ya kwacha.

A Chithyola amayankhula lachitatu pomwe amayankha zomwe anayankhula tsogoleri wa dziko lino professor Arthur Peter Mutharika pomwe amatsegulira zokambira za chi 52 ku nyumba ya malamulo.

Poyankhapo a Manamvekha ati ndi zoonadi kuti IMF ili dziko muno koma palibepo gwilizano wina uliwonse, thumwi za bungweli zabwera kudzangoona mmene dziko la Malawi likugwilira ntchito zake potukura chuma.A Mwanamveka ati koma ngati pangakhale gwilizano uliwonse ukhala wokomera a Malawi eni ake.

Ndipo sipikala wa nyumba ya Malamulo a Sameer Suleman auza a Chithyola kati lero lachinayi apereke umboni nyumbayi pa zomwe iwo amanenazo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *