Wolemba Raphael Likaka.
Nduna ya Maboma ang’ono ndi chitukuko chamadera akumudzi Dr Ben Phiri achenjeza makhonsolo kuti azigwiritsa bwino ndalama za Boma zopangira zitukuko.
Dr Phiri amayankhula izi mu mzinda wa Zomba pankumano womwe Unduna wao udakonza wokambirana ndi akulu akulu akhonsolo ya mzinda wa Zomba.
Iwo ati azachotsa ntchito munthu wina aliyense ogwira ntchito ku Khonsolo ya mzinda wa Zomba yemwe azapezeka atadya ndalama za Boma.
Ndunayi idati Mzinda wa Zomba ndi mzinda wakale kale koma sukutukuka choncho apempha akulu akulu akhonsoloyi kuti awonesetse kuti mzindawu ukumangidwa nyumba zamakono.
Pankhani ya mlatho wa Likangala kwa Mpondabwino omwe udawonongeka Dr Phiri anenetsa kuti aliyense amene adadya ndalama za mlathowu azibweze popeza udamangidwa mwachinyengo komanso osalimba.
“Unduna wanga suzalekelera aliyense okudya ndalama za Boma zopangira chitukuko.” Adatero Dr Ben Phiri.
Poyambilira Dr Phiri adayendera Zomba Stadium komanso zitukuko zina zomwe Khonsoloyi ikumanga.
Nduna ya maboma ang’ono ikuyendera makhonsolo kuti iwone momwe makhonsolo mdziko muno akugwilira ntchito.


