Yemwe adali wofalitsa nkhani za a police ku Zomba Police Station Inspector Patricia Sipiliano wamwalira.
Sipiliano wamwalira Lachitatu mamawa kuchipatala chachikulu cha Zomba atadwala nthawi yochepa.
Pakali pano thupi lamalemu Sipiliano akulisunga kuchipatala chachikulu cha Zomba.
Dongosolo loyika mmanda thupi lamalemu Sipiliano alilengezabe.


