Gulu la Kotale with Elder Matungulo lachezera odwala omwe akulandira chithandizo ku Cancer Centre mumzinda wa Lilongwe ndi cholinga chowalimbikitsa komanso kuwaonetsa chikondi ndi chisamaliro.
Wapampando wa gululi, a Harold Nason Gama, ati anaganiza zokachezera odwalawa chifukwa cha kufunitsitsa kwawo kuthandiza anthu omwe akudutsa m’nthawi yovuta ya matenda makamaka omwe amachokera kumadera akutali ndipo amakhala nthawi yaitali kuchipatala akulandira chithandizo.
Pa ulendowu, gululi linapereka zinthu zosiyanasiyana zothandizira odwalawa pa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku.
Zinthuzi zomwe mtengo wake wonse ukukwana K1.5 miliyoni, zikuphatikizapo sopo, shuga, mafuta ophikira komanso zinthu zina zofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku.
Gulu la Kotale with Elder Matungulo limachita maphunziro a Kotale kudzera pa lamya (online), ndipo lili ndi mamembala ochokera m’madera osiyanasiyana a m’dziko muno komanso m’mayiko ena kuphatikizapo South Africa.