Victor Musowa
Victor Musowa

PHUNGU WA MULANJE BALE AKUFUNA APHUNGU AKAMBIRANE ZA KUKWERA MTENGO KWA KATUNDU

Phungu wa dera la Mulanje Bale a Victor Musowa, apempha Sipikala wa nyumba ya Malamulo Catherine Gotani Hara kuti alole aphungu kukambirana nkhani yokhuza kukwera mtengo kwa katundu mziko muno.

Musowa wati mmene mitengo ya katundu ikukwelera zikuoereka chiphinjo kwa a Malawi osauka omwe akulephera kugula katundu ofunika pa miyoyo yawo.

“Ndi zodandaulitsa kuti boma sulikuchita kalikonse pa mmene katundu akukwelera mziko muno, choncho ndikupemoha kuti tikambirane za mmene tingachepetsere kukwera kwa katundu mdziko muno”, adatero Musowa.

Poyankhapo, mtsogoleri wa nyumbayi Richard Chimwendo Banda adati kovuta kutero chifukwa nduna yomwe imayamg’ana za nkhaniyi a Sosten Gwengwe sadafike kunyumbayi.

“Ndikadalempha kuti nkhaniyi iddzakambidwe ndunayi ilipo kuti pafunso ena akhoza kudzayankhidwa”, adatero Banda.

Komabe iye adati ngati Sipikala akuona kuti palibe vuto , nkhaniyi ikhoza kukambidwa mnyumbayi.

Mitengo ya katundu yakhala ikukwera mowirikiza mziko muno zomwe zaonjezera umphawi pakati pa a Malawi.

Kusowa kwa ndalama za  kunja ndi chimodzi mwa zomwe zikuchititsa kuti mitengo ya katundu izikwera.

Anthu ena azuzula boma chifukwa cholephera kukhwimitsa mchitidwe wogulitsa ndalama zakunja mopanda chilolezo.

Mchitidwewu ukukolezera kusowa kwa ndalama zakunja pamene anthu wamba ochita malondawa ndi amene akusunga ndalamazi mmalo moti zizikapezeka ku ma banki.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *