NETWORK TOWER YATHANDIZA ANTHU KULUMIKIZANA MOSAVUTA.

NETWORK TOWER YATHANDIZA ANTHU KULUMIKIZANA MOSAVUTA.

Phungu wa kuzambwe kwa Boma la Khata bay (Khatabay West) a Chrispine Mphande ati iwo ndi wokondwa kuti pepho lomwe anapepha nyumba ya malamulo tsopano lakwanilitsidwa lobweretsa tower ya TNM dera la Chitheka.

A Mphande amathokoza Boma mu nyumba ya malamulo pamene nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu amayankha mafuso kuchokera kwa aphungu a madera wosiyana siyana.

Amphande ati izi zikuthandiza anthu amadera ambiri kulumikizana mosamvuta mu thawi ina iliyonse.

” Anthu amamvutika kuti agule zipangizo za ulimi zotsika mtengo za (AIP) chifukwa zimawatengera kuti akwere phiri mtunda wa makilomita awiri Kuti akapeze network pofuna kupanga access kadi yogulira zipangizo” anatero a Mphande.

Koma iwo anapitiliza kuuza anduna azofalitsa nkhani Wolemekezeka a Moses Kunkuyu kuti a Boma achite machawi kubweretsanso tower ya Airtel Kuti afikile anthu onse kulumikizana mosamvuta mu mauthenga wosiyana siyana pozindikira kuti izi ndi njira imodzi ya chitukuko mdziko.

Koma poyankhapo nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu anati pasanathe masabata atatu tower ya Airtel ifika ku dera la Chitheka.

Wolemekezeka a Chrispine Mphande ndi mmodzi mwa makomishonala nyumba ya malamulo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *