ULAMULIRO WA MCP UDAWAPANGA CHIPONGWE ANTHU A KU ZOMBA- WATERO PHUNG

ULAMULIRO WA MCP UDAWAPANGA CHIPONGWE ANTHU A KU ZOMBA- WATERO PHUNG

Phungu wa dera la kumwera kwa mzinda wa Zomba a James Mpunga wati ulamuliro wachipani cha MCP udapanga nkhanza Pamodzi ndi chipongwe anthu a boma la Zomba.

Dr. Mpunga adati utsogoleri wa a Lazarus Chakwera ndi chipani chawo cha MCP udawonetsera chipongwechi potsegulira bwalo la za masewero losatha.Kutsekuliraku kudachitika patatsala masiku ochepa kuti anthu mziko muno akavote pachisankho chomwe chipanichi chidalephera.

Phunguyu adati chikhulupiliro cha anthu tsopano chili pa chipani cha DPP chomwe chidayambitsa ntchito yomanga bwaloli mchaka cha 2017.”Ife anthu a ku Zomba tasiya chikhulupiliro chathu chonse kwa mtsogoleri wathu Prof. Peter Mutharika kuti ndi iye atamalizitse ntchito yomwe adaiyamba yekha”, adatero Mpunga.Iye adati chinthu china chosonyeza kuti Mutharika ali ndi chidwi chotukula mzinda wa Zomba ndi kubwezeletsa  ma likulu a ma ofesi ena a boma komwe anali.

Ntchito ina yomwe ulamuliro wa MCP udalephera kumalizitsa kwa zaka zisanu ndi yomanga chipatala cha Domasi chomwe chili mdera la Zomba Malosa.

A Mpunga apemphanso nyumba ya malamulo ya ulendo uno kuti  ikambilane kuti chiyankhulo chomwe nyumbayi idzigwiritsa ntchito pokambirana chikhale choti anthu ambiri akhonza kumamva monga Chichewa Phunguyu adaonjezera kuti anthu mziko muno anada nawo kukhosi ulamuliro wa MCP ndipo ndizokaikitsa kuti udzabweleranso.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *