Khansala wachipani cha DPP wa Mpira Ward mu mzinda wa Zomba amusankha kukhala Mfumu ya Mzinda wa Zomba.
Khansala Jana wakhala pa udindowu atakhonjetsa Khansala Dickson Manda ndi mavoti 7 kwa 2 ndipo akhala Mfumu ya Mzinda wa Zomba kwa zaka ziwiri ndi hafu
Ndipo poyankhulapo atangosankhidwa Khansala Jana wati awonetsetsa kuti anthu okhala mu mzinda wa Zomba apindule ndi zitukuko zosiyana siyana ndipo wapemha anthu okhala mu mzindawu kuti azigwilira ntchito zachitikuko limodzi.
Ndipo khonsoloyi yasankhanso Khansala Anthony Gonani wachipani cha DPP wamdera la Masongola kukhala wachiwiri kwa Mfumu ya Mzinda wa Zomba.
Khansala Gonani wapeza mavoti 7 ndipo wakhala pa udindowu atagonjetsa makhansala ena awiri Monira Bakali ndi Juliana Fokoloni omwe apeza voti imodzi imodzi.
Khonsolo ya Mzinda wa Zomba ilindi makhansala asanu ndi anayi ndipo ili ndimadela awiri aphungu akunyumba yamalamulo.


