MWAMBO WOIKA MMANDA THUPI LA BRIGADIER CHANZA UCHITIKA LERO

MWAMBO WOIKA MMANDA THUPI LA BRIGADIER CHANZA UCHITIKA LERO

Wolemba Luke Magombo

Mwambo oika mmanda Brigadier Edger Venancio Chinangwa Chanza uchitika lero pa 17 November 2025 ku mudzi Kwa malemuwa Kwa Godeni, mfumu yaikulu Mulauli M’boma la Neno.

A Chinangwa adabadwa mchaka Cha 1971 mwezi wa July pa 13 ndipo amwalira pa 15 November 2025 atadwala Kwa nthawi yochepa mu mzinda wa Lilongwe ndipo thupi lawo latengeredwa kumudzi kwawo dzulo pa 16 November 2025.

Iwo agwira ntchito yoteteza dziko lino ngati msilikali komanso kukhala otetezera mtsogoleri wopuma wa dziko lino komanso wa chipani Cha MCP Dr Lazarus Chakwera zaka zisanu zapitazi.

A Chinangwa agwira ntchito ku Malawi Defense Force Kwa zaka zochuluka ndipo anali munthu odalirika ku ntchito kwawo. Iwo adalinso munthu othandiza anthu ovutita komanso osowa omwe amapempha thandizo Kwa iwo.

Mwambo onse wa maliro ukuyendetsedwa ndi asilikali ankhondo a MDF kuyambira kunyumba Kwawo ku Lilongwe, kuntchito kwawo ngakhalenso kuno Kwa Godeni M’boma la Neno

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *