BOMA LIKULIMBIKITSA MAKOLO KUTENGA GAWO PA ANA POTETEZA KACHILOMBO KA POLIO

BOMA LIKULIMBIKITSA MAKOLO KUTENGA GAWO PA ANA POTETEZA KACHILOMBO KA POLIO

Wachiwiri kwa Nduna ya Zaumoyo, a Charles Chilambula, apempha makolo ndi osamalira ana m’dziko muno kuti azindikire kufunika kotengera ana awo katemera wa matenda a polio kuti atetezedwe ku matendawa.

A Chilambula ananena zimenezi Lachiwiri pamwambo wokhakitsa gawo loyamba la kampeni wa katemera wa polio, womwe unachitikira ku sukulu ya pulayimale ya Makhetha ku Manda ambuzi m’boma la Blantyre.

Kampeniyi ikuyang’ana ana onse osakwanitsa zaka 10.
Iwo ananenanso kuti katemera ndi njira imodzi yofunika kwambiri poteteza ana ku matenda oopsa, ndipo apempha makolo onse kuti agwirizane ndi akatswiri azaumoyo powonetsetsa kuti ana onse akulandira katemerayu panthawi yake.

Pa mwambowu, bungwe la UNICEF linapereka njinga zamoto 17 ku ofesi ya zaumoyo ya boma la Blantyre (District Health Office).

Njinga zimenezi zidzithandiza akatswiri azaumoyo kufika m’madera osiyanasiyana mosavuta pofalitsa ntchito za umoyo ndi kupititsa patsogolo chisamaliro chaumoyo kwa anthu.

Gawo loyamba la kampeni ya katemera wa polio likuyembekezeka kuchitika kuyambira pa 11 mpaka 14 February, ndipo likukhudza maboma asanu ndi atatu omwe ndi Blantyre, Mwanza, Neno, Chikwawa, Nsanje, Thyolo, Zomba ndi Chiradzulu.

Boma likukhulupirira kuti kudzera mu kampeni imeneyi, ana ambiri atetezedwa ku matenda a polio, zomwe zingathandize kulimbikitsa thanzi la ana ndi tsogolo la dziko lonse.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *