Pamene boma likhale likukweza ma alawansi a ogwira ntchito ake kuchokera pa 1 July chaka chino, Mneneri wa boma Moses Kunkuyu wati ichi ndi chiyambi chabe cha zokoma zomwe Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera wakonza.
Kunkuyu yemwenso ndi nduna ya zofalitsa nkhani wati ogwira ntchito m’boma ayembekezere zambiri mu ulamuliro wa pulezidenti Chakwera.
“Kukwezedwa kwa ma alawansi a ogwira ntchito m’boma ndi zina mwa zomwe mtsogoleriyu wakhala akukonza pofuna kufewetsa miyoyo ya ogwira ntchito ake”, watero Kunkuyu.
Iye wati pamene pulezidenti Chakwera wakhala akuwauza a Malawi kuti adekhe, sikudali kungoyankhula chabe koma amadziwa chomwe amayankhula.
Mneneri wa bomayu wati mtsogoleri wa dziko linoyu akudziwa mavuto omwe a Malawi akukumana nawo omwe adadza kutsatira kutsika mphamvu kwa ndalama ya kwacha zomwe zidachititsa kuti mitengo ya katundu ikwere mdziko muno.
“Ngati gawo limodzi loonetsetsa kuti ogwira ntchito m’boma akusamalidwa, a Chakwera akweza ma alawansiwa pambuyo polembanso ntchito anthu ochuluka, kukweza mmaudindo ena mwa iwo komanso kuwaika pa ndondomeko ya zaumoyo (MASM)”, iye watero.
A Malawi ambiri kudzera pa masamba achezo kuphatikiza ogwira ntchito m’boma eni, ayamikira boma la malawi chifukwa chowaganizira ndi kukwezedwa kwa ndalamayi.
Nalonso bungwe loimira anthu ogwira ntchito m’boma la Civil Servants Trade Union (CSTU) lati lalandira nkhaniyi mokondwa kwambiri.
Mlembi wa bungweli a Titha Gomani wati izi zikuonetsa kuti boma lili ndi khutu lomvetsera zomwe ogwira ntchito ake akufuna pofuna kufewetsa miyoyo yawo.


