PHUNGU WA ZOMBA MALOSA WAYAMIKIRA BUNGWE LA UNDP CHIFUKWA CHOMANGA SCHEME MDERA LAKE.

PHUNGU WA ZOMBA MALOSA WAYAMIKIRA BUNGWE LA UNDP CHIFUKWA CHOMANGA SCHEME MDERA LAKE.

Phungu wa dera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta wayamikira Bungwe la UNDP mogwiridzana ndi Khonsolo ya Boma la Zomba chifukwa chomanga Nanyanga Sikimu (Solar Powered Irrigation Scheme) mudzi mwa Mkaju dera la Mfumu yayikulu Malemia Bomali.

Kwelepeta wati kumangidwa kwa Sikimu imeyi kuthandiza anthu amudzi mwa Mkaju kuti azikhala ndichokudya chokwanira chifukwa azikolola kawiri kapena katatu pachaka.

Iye watinso kubwera kwa sikumu imenyi kuthandizanso anthu a dera lake kuti azipeza ndalama zomwe ziziwathandiza pamoyo wao wa tsiku ndi tsiku komanso kulipilira ana sukulu chifukwa azitha kumagulitsa mbeu zina akakolola.

Pamenepa Kwelepeta walangiza anthu omwe azigwiritsa ntchito Sikimu ya Nanyanga kuti ayisamalire kuti anthu enanso mtsogolomu azathe kuyigwiritsa ntchito.

Kwelepeta adatinso apempha mabungwe omwe akugwira ntchito mdera lake kuti awathandidze alimi omwe azigwiritsa ntchito sikimuyi ndi mbeu yachimanga komanso mbeu zina zocha nsanga popedza alibe mbeu chifukwa chang’amba yomwe idavuta mdelari. 

“Mdera la Zomba Malosa limakhuzidwa ndi kutsefukira kwa madzi zomwe zimapangitsa kuti anthu asamakolole chimanga chokwanira choncho kumangidwa kwa Sikimu imeyi kuthandiza anthu kuti azipeza chokudya chokwanira.” Adatero Kwelepeta.

Ndipo pothililapo ndemanga Mai Cynthia Wochi amudzi mwa Mkaju adathokoza Bungwe la UNDP chifukwa chowamangira Sikimu yomwe idziwathandiza kuti adzikhala ndichokudya chokwanira.

Alimu 120 ndiwomwe azigwiritsa ntchito sikimuyi ndipo ndiyayikulu pafupi fupi 12 hekitala (hectares)

Bungwe la UNDP lamanga Nanyanga Sikimu (scheme) ndi thandizo landalama kuchokera ku Boma la Japan ndipo ndalama zomwe zagwira ntchito yomangira sikimuyi ndi 358 million kwacha.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *