Pamene chipani chotsutsa kunyumba ya Malamulo cha Democratic Progressive Party (DPP) chili kalikiliki kufuna yemwe atakhale wapampando wa Parliamentary Service Commission, chipanichi chikufuna kusinthanso mtsogoleri wotsutsa ku nyumbayi.
Sabata yatha, nyumbayi idakana kuvomereza dzina la phungu wa dera la Zomba Chingale Lonny Chijere Phiri pa udindo wa wapampando wa Parliamentary Service Commission.
Izi zidachitika aphunguwa atagwirizana zokana dzinali chifukwa chosowa mwambo akamayankhula mnyumbayi.
Mphekesera zikumveka kuti aphungu a chipanichi sakukhutira ndi mmene mtsogoleri wawo George Chaponda akugwirira ntchito mnyumbayi.
Zikumveka kuti aphunguwa akhala akukakamiza utsogoleri wa chipanichi kusankha munthu wina yemwe angalowe mmalo mwa a Chaponda.
Malinga ndi mamembala a chipanichi amene atitsina khutu, a Chaponda akumalephera kupereka mfundo zogwira mtima kuboma pa nthawi ya zokambirana mnyumbayi.
Mwachitsanzo, kusapezeka kwa a Chaponda pa nthawi yomwe nyumbayi idawapatsa mwayi woti apereke motion yokhuza kalembera wa unzika zidanyozetsa chipanichi.
Izi zikhoza kukhala kuti ndi zoona chifukwa mtsogoleri wachipanichi Peter Mutharika wasankha a George Chaponda kukhala mulangizi wawo pankhani yokonza ndondomeko za chipanichi.
Malinga ndi chikalata chomwe taona, a Mutharika asankhanso a Everton Chimulirenji kukhala mulangizi wawo pa nkhani zokopa anthu.
Ngati zingakhale chomwechi, ndiye kuti chipanichi chikhala kuti chasinthu utsogoleri wake otsutsa kunyumbayi kokwana kanayi mu chaka chino chokha.
Sabata yatha, nyumba ya Malamulo idakana kuvomereza dzina la phungu wa dera la Zomba Chingale Lonny Chijere Phiri pa udindo wa wapampando wa Parliamentary Service Commission chifukwa chosowa mwambo.
Pakadali pano, chipanichi chabalalika ndipo chikusowabe chochita ndi maudindo awiriwa.


