Bwalo la milandu m’boma la Nkhotakota lero lakana kutulutsa pa belo, a Emmanuel Matumba, omwe akuwaganizira kuti amafuna kuzembetsa mafuta a galimoto okwana malita 19, 800 kupita nawo m’dziko la Mozambique.
Bwaloli lakananso kupereka belo kwa Juwawo Mndala mzika ya m’dziko la Mozambique pa mlandu omwe akuwaganizira kuti analowa m’dziko muno opanda zikalata zowayenereza.
Mndala ndi yemwe anayenera kunyamula mafutawa omwe ndi Diesel komanso Petrol ngati dalayivala ndi boti lawo pa nyanja ya Malawi.
Aulerious Phukaphuka womwe akuyimira boma pa mulanduwu ati Matumba sakuyenera kupatsidwa belo chifukwa ndi mzika ya m’boma la Nkhotakota, choncho atha kusokoneza kafukufuku yemwe apolisi akuchitabe pakalipano.
Yemwe akuyimira oganiziridwayu Silvester Ayuba James, sanapezeke ku bwaloli koma anapereka pempho kuti mulanduwu utha kumvedwa.
Bwaloli laimitsa Kaye mulanduwu mpaka pa 8 April chaka chino, ngati tsiku lomwe lidzamve pempho la boma kuti mulanduwu ukamvedwe ku bwalo la milandu la Mtosa m’dera la Benga Kwa Mfumu yaikulu Mwadzama komwe kunachitikira nkhaniyi.
Izi ati zithandizira kuti mboni za boma zikapelekere umboni wawo moyenera.
Woweruza mulandu Stonard Nthala ndi yemwe akumva mulanduwu ndipo a Clement Ng’ambi ndiomwe akuyimira bungwe la MERA.


