NDUNA ILONJEZA KUPITITSA PATSOGOLO NTCHITO ZA ACHINYAMATA

NDUNA ILONJEZA KUPITITSA PATSOGOLO NTCHITO ZA ACHINYAMATA

Nduna yoona za achinyamata, masewero ndi chikhalidwe, a Patricia Wiskes, yalonjeza kupititsa patsogolo ntchito zonse zokhudza achinyamata.Iwo akuti izi ndi zothandiza kaamba koti, anthu 7 mwa 10 alionse ndi achinyamata.Choncho ndi kofunikira kuti achinyamatawa alandire zofuna zawo komanso kuti ntchito zawo zidziyenda mu nthawi yake.A Wiskes amayankhula izi atakayendera ofesi za National Youth Council of Malawi (NYCOM) mu mzinda wa Lilongwe. Mkulu wa NYCOM, a Rex Chapota, wati kubwera kwa ndunayi ku maofesiwa kukutanthauza kulimba kwa ubale wa mbali ziwirizi komanso chitukuko cha ntchito za achinyamata m’dziko muno. M’malo mwake, a Chapota anathokoza mtsogoleri wa dziko lino, a Arthur Peter Mutharika, kaamba kosankha a Wiskes ngati nduna mu unduna wa achinyamata, masewero komanso chikhalidwe.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *