HOPESON NOTICE WAGONJETSA LIMANI ROTCHA PA MASEWERO A KICKBOXING

HOPESON NOTICE WAGONJETSA LIMANI ROTCHA PA MASEWERO A KICKBOXING

Hopeson Notice wochokera ku Blantyre Youth Center tsopano ndi katswiri wamasewero a Kickboxing mdziko muno.

Notice wakhala katswiri atagonjetsa nyamata waku Zomba Limbani Rotcha mundime yotsiriza ya nambala 7 pamasewero omwe adachitika la Mulungu ku China Complex mu mzinda wa Zomba.

Poyankhula atapambana pampikisanowo Notice adati chiyambire kumenya masewerowa sadaluzepo ndipo chinsinsi chake ndikulimbikira ku pokonzekera.

Iye adatinso adamumenya Limbani Rotcha chifukwa cha mau achipongwe omwe adayankhula masewerowo asadayambe okuti iye azamuyika bokosi chifukwa azapita kwao ali maliro.

Iye adati ngakhale adapambana masewerowo koma sadali okhutitsidwa ndi ndalama yokwana 150,000 yomwe adalandira chifukwa panthawi yomwe amakonzekera mpikisanowo adawononga ndalama zambiri.

Notice yemwe amelemera 76kg adati masomphenya ake akufuna kuzayamira dziko muno pamasewero a kickboxing ndi maiko ena mtsogolo muno.

“Ndithokoze a Bungwe la Malawi Kickboxing Association chifukwa chokonza masewera amenewa chifukwa atipangitsa kuti osewera tizilimbikira.” Hopeson Notice adatero.

Masewero akulu a kickboxing asadayambe kudalinso akalambula bwalo omwe ndiwosapitilira kulemera 60kgs pomwe nyamata ochokera ku Club ya MUBAS, Dan Disi adagonjetsa nyamata wochokera kwa Bvumbwe, Bahat Chakondwa

Ndipo masewero a kickboxing atsikana Sakina Ibrahim wochokera ku Lilongwe adagonjetsa Luthando Sikwese ochokera ku Mzuzu

Ndipo poyankhula atatha masewerowo, President wa Malawi Kickboxing Association Benedict Tsinde adati adali wokondwa momwe masewerowo adayendera chifukwa achinyamata akulimbikira ndipo akufuna kuti mtsogolo muno azizamenyana ndi maiko aku Ulaya.

Iwo adati masewero amenewa awathandiza kuti asankhe osewera omwe azapikitsane ndi anzawo ochokera maiko a Zimbabwe ndi Mozambique pa 6 July chaka chino.

Mau ake ogwirizira udindo wa Chief Executive Officer ku Bungwe la Malawi National Council of Sports Ivy Chinangwa adati ndiwosangalala kwambiri chifukwa awona luso la kickboxing kuchokera kwa achinyamata ndi zawalimbikitsa kuti Bungwe lawo lipitilize kuthandiza masewerowa.

Iwo adati koma adali okhumudwa chifukwa atsikana ambiri sadatenge nawo mbali

Ma Club ochokera ma Boma a Zomba, Lilongwe, Blantyre, Mzuzu, Thyolo komanso Mangochi ndiwomwe adatenga nawo mbali pamasewerowo

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *