KOMITI YA ZA UMOYO YA NYUMBA YA MALAMULO YATI BOMA LIPITILIZE GANIZO LOKHALA NDI ZIPINDA ZOLIPIRA ZA MA BOMA

KOMITI YA ZA UMOYO YA NYUMBA YA MALAMULO YATI BOMA LIPITILIZE GANIZO LOKHALA NDI ZIPINDA ZOLIPIRA ZA MA BOMA

Komiti ya nyumba ya malamulo ya za umoyo yati boma likufunika lichilimike pa ndondomeko zina zomwe zingathandize kuti zipatala mudzikhala thandizo lokwanira popeza mwa ilo lokha.

Wapampando wa komitiyi a Anthony Masamba amanena izi pomwe amapereka lipoti nyumbayi pazimene komitiyi yapeza poyendera zipatala komaso kukumana ndi akadaulo pa za umoyo.

Mwa zina komitiyi yapeza kuti kukhala ndi zipinda zolipira ku zipatala za ma Boma kutha kuthandiza kuti zipatala zidzikwanitsa kupeza thandizo palokha, chifukwa alipo ena amene ali ndi kuthekera kolipira paokha komaso ena amane amagwilitsa ntchito ndondomeko ya Masm, potengera kuti zipatala za Boma zili ndi ukadaulo komaso zida zamphamvu zothana ndi matenda ambiri.

Izi zadza potengera kuti ambiri omwe amatithandiza monga aku America anasiya kupereka thandizo lawo

“Ndondomeko yolipira ndi yabwino kwambiri koma isapangitse kuphinja omwe alibiletu thandiza ku ma Bomako” anatero a Masamba.

Iwo anaonjezera kuti unduna wa za umoyo ukuyenera kuika misomkho pa zinthu monga Suga, mchere, mowa komaso Shisha kuti izi ndi zomwe zimabweretsa matenda a chifuwa chachikuru cha TB, chomwe chimafuna ndalama zambiri kuti anthu athandizike.

Poonjera izi nduna ya za umoyo a Madalitso Baloyi anati iwo anaona kuti njirayi ndiyothandiza kukwaniritsa kupeza zithandizo za kuchipatala pa lokha.

“mwa chitsazo chipatala cha Kasungu pa mwezi chimapanga ndalama zopitilira 40 million zomwe zingathe kuthandizira kukoza ma ambulances, ma bed, wheelchair, mipando ndi zina zambiri choncho kukhala ndi zipinda zolipira ndi ganizo labwino” anayakhula choncho a Baloyi.

Unduna wa za umoyo umakumana ndi mamvuto ambiri kuti anthu apeze thandizo ku zipatala zosiyanasiyana.

Koma yemwe amayankhulira ku za umoyo a Goerge Jobe anati njira izi ndi zabwino koma pakufunika kuunika njira zonse kupewa kuphinja anthu omwe alibiletu thandizo.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *