ACB muli kuti? Afunsa Namalomba pa nkhani za katangale
Nduna yoona za Zofalitsa Nkhani ndi Ukadaulo wa Zamakono, Dr Shadreck Namalomba, yafunsa komwe kuli bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB), ponena kuti anthu omwe ali ndi umboni wa katangale m’boma ayenera kupereka umboniwo ku bungweli m’malo mopita nawo ku Nyumba ya Malamulo.
Polemba pa tsamba lake la Facebook, Dr Namalomba wanena kuti Nyumba ya Malamulo si bungwe lomwe limagwira anthu omwe akuganiziridwa kuti achita zolakwa, popeza ntchito yofufuza milandu ya katangale ili m’manja mwa ACB, pomwe makhoti ndi omwe ali ndi udindo woweruza milanduyo.
“Tidamenyera nawo nkhondo chipanichi, sitingayang’anire mphekesera za katangale zichimalize. Katangale ndi mlandu waukulu, si nkhani yongolankhula,” adatero Dr Namalomba.
Pakadali pano, Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sameer Sulemani, wanenanso kuti anthu ena m’boma ali ndi mphamvu zazikulu. Komabe, iye wanena kuti monga Msilamu, ndi wokonzeka kufera anthu a Malawi, potsatira zomwe akukhulupirira kuti ndi mfundo za chipembedzo chake zokhudza kudzipereka pa ntchito yaNkhaniyi ikubwera pamene pali mkangano wokhudza momwe milandu ya katangale iyenera kufufuzidwira komanso udindo wa mabungwe osiyanasiyana a boma polimbana ndi mchitidwewu.