FRANK CHITEMBEYA AMEMA ANTHU A M’BUKA KUDZAMUPATSA VOTI

FRANK CHITEMBEYA AMEMA ANTHU A M’BUKA KUDZAMUPATSA VOTI

Pamene kwatsala masiku ochepa kuti anthu mziko muno apite akaponye voti pa 16, September, Frank Chitembeya apempha nzika za m’dera la M’buka kuti ziwapatse mwayi woyimilira iwo mu Nyumba ya Malamulo ngati phungu.

Chitembeya limodzi ndi omwe akuimila ngati councillor a ku Mwenyekondo ward a Dalitso Chingoli komanso a Gregory Mwanza omwe akuimila ku Kasemba Ward — ayendera ntchito zosiyanasiyana zomwe akhala akupanga m’derali, makamaka zomanga milatho.

Atayendera pa Bridge la Mitengo, Chitembeya anati: “Mlathowu usanamangidwe, anthu ambiri anataya miyoyo, ena nawonso anavulala chifukwa chosatha kudutsa. Ichi ndichifukwa chake tikugwirizana ndi ma councillor komanso mafumu athu kuti titukule malo osiyanasiyana m’dera lino.”

Iwo ananenanso kuti sukulu zambiri m’derali ndi kutali moti ana ambiri amaoloka mitunda yayitali kuti afike kusukulu. “Tikufuna izi zikhale mbiri yakale. Cholinga chathu ndi kumanga sukulu zambiri kuti ana aphunzire pafupi ndi kwawo.”

Mwa masomphenya awo, Chitembeya adalumbira kuti akawasankha, adzamanga chipatala, misewu ya tala, komanso kulimbana ndi umbava mwa kupatsa achinyamata ndi amayi zipangizo ndi ndalama zoyambira mabizinesi.

Nzika za m’derali zanena kuti zikudabwa chifukwa Chitembeya sanayime kale pa chisankho, popeza ntchito zomwe akugwira zikuwoneka.

Kuphatikiza apo, iwo anatsimikiza kuti masomphenya a chipani cha UTM kudzera mwa mtsogoleri wake Dr. Dalitso Kabambe, akuwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro choti dela la M’buka likhoza kusintha kukhala dera lolozeka chifukwa ili pafupi ndi tauni ya Lilongwe koma chitukuko chake chili m’mbuyo.

Pa msonkhanowu, mafumu a ku Mwenyekondo ndi ku Mitengo anapereka mawu owayamikira Chitembeya pa ntchito zawo. Iwo anapemphanso anthu a m’dera kuti apereke voti kwa iwo komanso ma councillor ake awiri — Gregory Mwanza ndi Dalitso Chingoli.

M’buka ili mu dera la 36, pafupi ndi tauni ya Lilongwe.

Leave a Comment

Comments

No comments yet. Why don’t you start the discussion?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *