Osewera mpira wa miyendo a dziko lino, Flames, agonjetsedwa 3-1 ndi Angola pamasewera a AFCON 2027 qualifiers omwe anachitikira pa Estadio 11 de Novembro ku Luanda usiku wa pa 6 October 2026.
Angola inayamba masewerawa mwamphamvu ndipo patangodutsa mphindi zitatu zokha, Mendes anatsegula chitseko cha zigoli pambuyo poti osewera a Angola adagwirizana bwino ndi kupatsirana mpira kothamanga kwambiri komwe kunapangitsa a Malawi Kusowa mtendere mmasewerawa.
Zinali zovuta kwa Flames kumayambiriro kwa masewerawa, pomwe mpaka mphindi 20 Malawi inali isanawombere mpira wolunjika pa golo pomwe panali otchinga pagolo wa Angola.
Angola inalamulira kwambiri mpira ndi 77%, pomwe Malawi inali ndi 23% yokha.
Mphindi ya 40, kaputeni wa Angola Mabululu anawonjezera chigoli chachiwiri ndi mutu kuchokera pa corner kick zomwe zinagwetsa ulesi osewera a team ya Malawi.
Angola inapitiriza kupeza mipata mosavuta m’gawo la Malawi, zomwe zinapangitsa goalkeeper wa Flames, William Thole, kukhala wotanganidwa kwambiri.
Angola inapitirizanso kupeza ma corner kick ambiri, zomwe zinasonyeza momwe inalamulira ndikulavula malawi amoto mmasewerawa.
Koma pomwe zimaoneka kuti Angola ipita ku nthawi yopuma ikutsogola 2-0, Patrick Mwaungulu anabwezeretsa chiyembekezo cha Malawi ndi free kick yabwino mphindi yomaliza ya first half.
Mpirawo unakhudza wosewera wa Angola ndipo chigoli chinaperekedwa ngati own goal.
Choncho, Angola inapita ku nthawi yopuma ikutsogola 2-1.
Mu second half, Flames inayamba kusewera bwino komanso kukhala yokhazikika poyerekeza ndi mmene inayambira masewerawa.
Mphunzitsi wa Malawi, Pasuwa, analowetsa osewera atsopano monga Mbulu, Singo ndi Malango, ndipo osewerawa adagwirizana bwino ndi anzawo zomwe zinathandiza Flames kuyamba kulamulira masewerawa komanso kupeza chidaliro.
Ngakhale Malawi inayamba kukhala ndi mpira kwambiri, Angola inapitiriza kutsogola ndi 76%, pomwe Malawi inali ndi 24%.
Koma pomwe Flames inafunafuna chigoli chofananirana mphamvu, Angola inachinyanso chachitatu nkumasiyana zigoli ziwiri ndikupangitsa kuti masewerawo akhale 3-1.
Pofika mphindi ya 86, Angola inali itawombera ma bomba 18 olunjika pachipata, ndipo atatu mwa iwo adasanduka zigoli. Malawi inali itangowombera ma bomba 5.
Angola 3-1 Malawi.