NDENDE YA ZOMBA NDI BVUMBWE YAFIKA M’NDIME YOTSILIZA YA MPIKISANO WA CHESS

Malawi yachita bwino kwambiri pa mpikisano wa chess wa pa intaneti wa akaidi ochokera m’mayiko osiyanasiyana, pomwe ndende ya Zomba Central ndi Bvumbwe young offenders rehabilitation centre (YORC) onse akwanitsa kulowa mu ndime yotsiliza kutsatira kuchita bwino kwawo.

Gulu la Zomba Central Prison, lomwe likupikisana pansi pa dzina la Malawi 2, lapeza malo achiwiri m’gulu lachisanu ndi chimodzi ndi mapointi 10.
Pomwe gulu la Bvumbwe YORC, lomwe likudziwika kuti Malawi Youth 2, lachita bwino kwambiri potsogola m’gulu lake osagonjetsedwa, litapambana magulu ochokera ku Kenya, Serbia ndi Romania.

Mneneri wa Zomba Central Prison, Sergeant Yusuf Daniel Ayuba, wayamikira maguluwa chifukwa cha khama lawo, ponena kuti kupambana kumeneku ndi chinthu chofunika kwambiri ngati dziko.

Ayuba wafotokozanso kuti masewera a chess amathandiza akaidi kukulitsa luso loganiza mozama, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kusintha moyo wawo.

Magulu onsewa akuyembekezeka kupikisana mu ndime yotsiliza lero pa mpikisano womwe cholinga chake ndi kulimbikitsa kusintha kwa makhalidwe akaidi, kuphunzira komanso mgwirizano pakati pa mayiko kudzera m’masewera a chess.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *