Amayi oposa 500 mumzinda wa Zomba aphunzitsidwa maluso ochitira mabizinesi ang’onoang’ono pofuna kuwathandiza kuti azidzidalira pazachuma.
Amayiwa, omwe ndichokera m’madera atatu aphungu mumzindawu, aphunzitsidwa kupanga sopo, kupanga peanut butter, mafuta ophikira komanso kasamalidwe ka ndalama.
Maphunzirowa achitikira pa bwalo la Gymkhana Ground ndipo atsogoleredwa ndi bungwe la CTS courier komanso Small and Medium Enterprises Development Corporation (SMEDCO).
Mkulu woona za malonda ndikufalitsa nkhani ku pakampani ya CTS Courier, Vannessa Kameza, wati kampaniyi ikukonzekera kukhazikitsa magulu a amayi ochitira mabizinesi pamodzi kuti awathandize kupeza ndalama zoyambira mabizinesi komanso kukulitsa mabizinesi awo.

Kameza wawonjezeranso kuti maphunzirowa akuyembekezeka kufalikira m’mizinda ya Lilongwe ndi Mzuzu pakati pa mwezi wa January ndi March chaka chamawa.
Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa dera la Zomba Malosa, Grace Kwelepeta, walimbikitsa amayiwa kugwiritsa ntchito maluso omwe aphunzira poyamba mabizinesi komanso kutengerapo mwayi pa ngongole za thumba la Constituency Development Fund (CDF).
Mmodzi mwa ophunzira, Emily Bwalambo wa ku Zomba Malosa, wati akufuna kuyamba bizinesi yopanga peanut butter ataphunzira malusowa.
Kumbali yake, mkulu woona zofalitsa nkhani ku SMEDCO, Micah Nthere, wati cholinga cha maphunzirowa ndi kuthandiza amayi kuti azitha kudzipezera ndalama komanso kukhala odziyimira pawokha pazachuma.