Apolisi KU ZOMBA AMANGA ANTHU 27 CHIFUKWA CHA MILANDU YOSIYANA SIYANA PA ZIKONDWELERO ZOKUMBUKIRA UFULU

Apolisi a ku Zomba amanga anthu 27 pa milandu yosiyanasiyana kutsatira mumzinda wa Zomba ndi madera ozungulira pa nthawi ya chikondwerero pa tsiku lokumbukila Ufulu odzilamulila tokha.

Malinga ndi Wachiwiri kwa Mneneri wa Apolisi ku Zomba, constable Andrew Mwale, anthuwa amangidwa pa milandu yokhala ndi mafuta a petro popanda chilolezo chovomerezeka, kuchita zinthu zomwe zingayambitse kusokoneza bata m’madera, juga, komanso kuyendetsa mabizinesi ogulitsa mowa popanda zilolezo zovomerezeka.

Pakadali pano, onse omwe amangidwawo ali m’ndende ya apolisi ndipo akayankha milandu yawo kukhoti akamaliza njira zonse zofunika zamalamulo.

Apolisi a ku Zomba atsimikiziranso kudzipereka kwawo posunga mtendere, malamulo ndi chitetezo cha anthu.

Alimbikitsanso nzika kuti zipitirize kugwira ntchito limodzi ndi apolisi popereka malipoti pa milandu pa nthawi yake kuti zithandize kupewa ndi kuthana ndi uchifwamba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *