NRB IYAMBA GAWO LACHINAYI LA KALEMBEDWE KA ANA M’MABOMA ANAYI

NRB IYAMBA GAWO LACHINAYI LA KALEMBEDWE KA ANA M’MABOMA ANAYI

Bungwe Loona za Kalembera wa Anthu (NRB) liyamba gawo lachinayi la ntchito yolembetsa ana m’maboma a Mulanje, Thyolo, Chikwawa ndi Nsanje kuyambira Lachiwiri, pa 28 Julayi 2026.

M’chikalata chomwe bungweli latulutsa, chosainidwa ndi Mlembi Wamkulu wa NRB, Patrick Machika, akuti ntchito ya masiku 10, yomwe idzatha pa 6 Ogasiti 2026, ikufuna kulembetsa ana osakwanitsa zaka 16 komanso kuwapatsa ziphaso zobadwa.

Pa ntchitoyi, NRB idzalembetsanso achinyamata azaka 16 ndi 17 kuti apeze ziphaso za unzika (National ID).

Makolo akulimbikitsidwa kupita ndi ana awo ku masukulu a pulaimale a boma komwe kulembetsaku kudzachitikire kuti akalandire ziphaso zobadwa.

Achinyamata azaka 16 ndi 17 akuyenera kupita ku malo oyandikana nawo a Teacher Development Centres (TDCs) kuti akalembetse ziphaso za unzika.

NRB yati cholinga cha ntchitoyi ndi kuonetsetsa kuti ana onse m’dziko muno akhale ndi zikalata zovomerezeka zomwe zingawathandize kupeza ntchito zosiyanasiyana za boma ndi zachitukuko.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *