Mtsikana wa zaka 15, Grolia Time, wa mmudzi mwa a Matope, kwa mfumu yaikulu Sandrack m’boma la Chiradzulu, wamwalira atamwa chinthu choopsa chomwe akuganiziridwa kuti anapatsidwa ndi mayi ake.
Malinga ndi James Molesi, yemwe ndi agogo a mtsikanayu ndipo ndi amene anauza apolisi za nkhaniyi, Grolia, yemwe anali ndi vuto la maganizo, anayamba kudwala atabwerera kuchokera ku maliro ku dela Chitera.
Molesi wati ali m’njira yobwerera, mayi ake a Grolia, Nduzayani Molesi, wazaka 31, anaima pa Mbulumbuzi Trading Centre ndipo akuti anagula mapiritsi a mankhwala ophera tizilombo.
Atafika kunyumba, Nduzayani analowa m’nyumba, n’kuitana Grolia ndipo anamupatsa zovala zatsopano zomwe akuti anali atamugulira.
Patangopita nthawi yochepa, Grolia anatuluka akusanza kuseli kwa nyumba.
Ngakhale Molesi anati mtsikanayu apite naye kuchipatala, akuti Nduzayani anakana.
Komabe, pamene matenda anakulirakulira, Grolia anatengedwa kupita ku Milepa Health Centre komwe analandira thandizo, koma
Grolia anapitirizabe kudandaula za kupweteka m’mimba ndipo posakhalitsa anamwalira.
Kutsatira imfayi, apolisi a Chiradzulu anapita kukamanga mai Nduzayani komanso kutengera mtembo wa Grolia ku Chiradzulu District Hospital kuti akafufuze chomwe chinayambitsa imfa.
Zotsatira za postmortem zasonyeza kuti Grolia anamwalira chifukwa cha poizoni wa organophosphate, yemwe amagwiritsidwa ntchito popanga mankhwala ophera tizilombo.
Apolisi atsegula mlandu ndipo Nduzayani ali m’manja mwa apolisi pomwe kafukufuku ukupitilira.