DAYOSIZI YA UPPER SHIRE YA MPINGO WA ANGLICAN YASONKHANITSA ANSEMBE KU CHILEMA POLIMBIKITSA MGWIRIZANO WA UTUMIKI

Dayosizi ya Anglican ya Upper Shire lero yayamba msonkhano wa ansembe wa masiku angapo (Clergy Retreat) ku Chilema m’boma la Zomba, womwe cholinga chake ndi kulimbikitsa umodzi, ubale komanso mgwirizano pakati pa ansembe omwe akutumikira m’maparishi osiyanasiyana m’dayosiziyi.

Bishopu wa Dayosizi ya Upper Shire, William Joseph Mchombo, wati msonkhanowu wabweretsa pamodzi ansembe kuti apemphere limodzi, alimbikitsane komanso agawane mavuto omwe akukumana nawo m’maparishi awo osiyanasiyana.

Bishopu Mchombo awonjezera kuti msonkhanowu ukupatsa ansembe mwayi wophunzirana, kulimbikitsa ubale wawo komanso kukambirana nkhani zomwe zikukhudza Mpingo ndi anthu omwe amawatumikira.

Iwo ati dayosiziyi ikukhulupirira kuti msonkhanowu uthandiza kuti ansembe onse azikhala ndi kumvetsetsa kofanana pa ntchito ndi cholinga cha Mpingo, ngakhale akutumikira m’maparishi osiyanasiyana.

Mchombo watinso akuyembekezera kuti msonkhanowu ulimbikitsa kukula mwauzimu, kulimbitsa mgwirizano pakati pa ansembe komanso kupititsa patsogolo ntchito ya utumiki m’Dayosizi ya Upper Shire.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *