Membala wa Nyumba ya Malamulo wa Blantyre City South Lunzu, a Hon.
Veronica Ndalama, lero apereka galimoto yonyamula katundu ya matani awiri kwa anthu a m’dera lawo.
Polankhula pamwambo wolanditsa galimotoyo, a Ndalama ati galimotoyi ithandiza kuchepetsa mavuto a mayendedwe omwe anthu m’derali akhala akukumana nawo kwa nthawi yayitali.
Malinga ndi a Ndalama, galimotoyi idzagwiritsidwanso ntchito pa ntchito zachitukuko m’dera lawo komanso kunyamula anthu pa nthawi ya maliro.
Anthu komanso atsogoleri a chikhalidwe m’derali ayamikira a Ndalama chifukwa cha thandizoli, ponena kuti galimotoyi ithandiza kwambiri anthu am’derali.
Galimotoyi, yomwe ili ndi chithunzi cha a Hon. Ndalama komanso mauthenga a kampeni, inalandidwa ndi chisangalalo ndi anthu a m’derali omwe anasonkhana ku Lunzu kuti alandire galimotoyo.