Bishop Alfred Mateyu Chaima Lamungu adatsogolera mwambo wa missa yotsekulira guwa lopemphelera la panja komanso mwambo wa ulimbitso omwe ukuchitikira ku Zomba Cathedral.
Pamwanbo wotsekulira guwali, akhristu opitilira 300 adalandiranso sacrament la Ulimbitso.
Poyankhula pamwanbowo Bishop Chaima adathokoza akhristu onse omwe adatengapo mbali yothandiza kumanga guwali ndi chuma chawo komanso mphamvu zawo.
Iwo adapemphanso makolo ana omwe alandira ulumbitso kuti aziliwambikitsa kupemphera kuti azakhale ana odalilika mumpingo patsogolo.
Poyankhulapo, Professor Francis Moto yemwe ndi wapampando wa komiti yomwe imawongolera kamangidwe ka guwalo adayamikira akomiti anzawo chifukwa chamgwirizano omwe udalipo panthawi yomwe guwalo limamangidwa.
Ntchito yomanga guwali lidatsekuliridwa (launch) pa 17 October chaka cha 2024 ndipo ndalama zokwanira 71 million kwacha ndizomwe zagwiritsidwa ntchito.
Ena mwa akulu akulu omwe adafika kumwambowo ndi monga Vice Chancellor wa Catholic University Professor Francis Moto, Dr Peter Namphande m’phunzitsi waku University ya Malawi, ma sister ampingo wakatolika komanso akhristu ochuluka eni ake.