GERTRUDE MUTHARIKA APEMPHA MGWIRIZANO WA AMAYI PA UKHONDO NDI CHITUKUKO

Mkazi wa Mtsogoleri wa dziko lino, a Gertrude Mutharika, apempha amayi onse m’dziko muno kuti agwirizane pothana ndi mavuto a ukhondo komanso kulimbana ndi matenda opeweka.

A Mutharika ananena izi lero ku Lilongwe pamwambo womwe bungwe lawo la Beautify Malawi (BEAM) Trust linasainirana mgwirizano ndi bungwe la amayi a ku Malawi Police Service Women Welfare.

Iwo ati mgwirizanowu uthandiza kulimbikitsa amayi kutenga nawo mbali pa ntchito za chuma, ukhondo komanso chitukuko cha dziko.

Mkazi wa Mtsogoleri wa Apolisi, a Rhoda Longwe Luhanga, ayamikira mgwirizanowu, ponena kuti ndi nsanamira yofunika kwambiri polimbikitsa ndi kupititsa patsogolo ntchito za amayi.

Pamwambowu, a Gertrude Mutharika aperekanso ndalama zokwana K10 miliyoni ku bungwe la amayi a ku Malawi Police Service, pamodzi ndi makina osokera asanu, pofuna kuthandiza pa ntchito zawo zopititsa patsogolo moyo ndi chuma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *